"TAGWIRIZANA KUTI TIWINE TIKACHISIYE KWA A MPINGANJIRA" - CHAZIYA
Mtsogoleri wa osewera kutimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Lawrence Chaziya, wati osewera onse agwirizana kuti ayesetse kuwina chikho chimenechi ndi cholinga choti akachisiye kwa mtsogoleri wa timuyi Thomson Mpinganjira.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero amu ndime yotsiriza ya Castel Challenge yomwe iliko loweruka pa bwalo la Bingu pakati pa timuyi ndi Mzuzu City Hammers.
Iye wati chikhala chinthu chokoma kwambiri kutenga chikhochi chifukwa ndekuti chipereka chilimbikitso kwa osewera kuti chaka cha mawa adzachitenso bwino mu zambiri.
Iye anati: "Ifeyo takonzekera bwino kwambiri ndipo tagwirizana kuti titenge ichichi tikachisiye kwa a Mpinganjira. Molalo ili pamwamba ndipo izizi zitheka ndithu."
Ichi chitha kukhala chikho choyamba mu zaka ziwiri ku mbali ya Manoma omwe anachoka chaka chatha opanda chikho ndipo komaliza munali mu 2022 pomwe anatenga Airtel Top 8 pansi pa Mark Harrison.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores