"KUCHOKA KWA MTONDAGOWA NDI MWAKAPENDA KUNATISOKONEZA" - MPULULA
Mphunzitsi watimu ya Mighty Tigers, Leo Mpulula, wati ligi ya chaka cha 2024 inali yovuta kwambiri poti timu yake imangokwanitsa kupambana ndi chigoli chimodzi chokha basi ngakhale kuti amapeza mipata yochuluka kwambiri.
Iye amayankhula pomwe amaunguza momwe timuyi yachitira mu chakachi ndipo sanabise Chichewa koma kunena kuti timuyi inavutika kwambiri mu chakachi.
Iye wati kuchoka kwa osewera monga Bright Mtondagowa komanso Iven Mwakapenda omwe anapita ku maphunziro a zandende pomwe ligi inangoyamba kumene zinawasokoneza kwambiri.
"Tinatayanso Bright Mtondagowa ndi Iven Mwakapenda omwe anali osewera anga omwe ndimawadalira kwambiri chifukwa amayamba mmasewero athu koma tinasewerabe mpaka sinatuluke mu ligi." Anatero Mpulula.
Iye wati timuyi ikuyenera kuchilimika ndi kukonza mavuto awo mu chaka cha 2025 kuti isadzakhalenso ndi phuma loti akhonza kutuluka mu ligi chaka chino.
Timuyi inamaliza pa nambala yachikhumi nd
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores