"TIKUFUNA TIFIKE MU NDIME YOTSIRIZA" - CHIMKWITA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Karonga United, Christopher Chimkwita, wati timu yake ikuyang'ana kuti ifike mu ndime yotsiriza ya mpikisano wa Castel Challenge poti ndi zomwe akonza kuti akwanilitse mu mpikisanowu.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Mzuzu City Hammers mu ndime ya matimu asanu ndi atatu a mpikisanowu pomwe wati akudziwa kuti akhale masewero ovuta kwambiri koma ayesetsa kuti apambane.
Iye wati anakwanilitsa kale kufika mu ndime ya matimu anayi a mpikisano wa FDH Bank ndipo akufuna achitenso chimodzimodzi kapena zikaphweka afike ndime yotsiriza.
"Tikufuna titafika mu ndime yotsiriza kapena zikavuta mu ndime ya matimu anayi mu ligi tinayesetsa kufika mu matimu asanu ndi awiri nde tikafika ndime yotsiriza zitikomere kwambiri." Anatero Chimkwita.
Masewerowa aseweredwe pa bwalo la Karonga lomwe ndi pakhomo pa timu ya Karonga United ndipo opambana afika mu ndime ya matimu anayi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores