"TIKADAGWIRAGWIRA KUTI TIFIKE PENIPENI" - CHIMKWITA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Karonga United, Crespo Chimkwita, wati timu yake tsopano ikuoneka kuti yagwirana pomwe mu chigawo chachiwiri cha ligi akuchita bwino ndipo akukonzabe kuti ifike penipeni polimba bwino.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Mighty Tigers pa bwalo la Kamuzu lachitatu ndipo iye wati timu yake inavutika mchigawo choyamba poti anyamata ake ambiri anapita ku matimu ena.
"Osewera ena anali asanagwirane poti anali achilendo kutimuyi koma tsopano akuoneka kuti pano ali bwino kwambiri, tikugwirana nde tikadakonza kuti tifike penipeni pabwino." Anatero Chimkwita.
Iye wadandaulanso kuti timu yake ikuyenda kwambiri pa masewero awo komabe poti mpira wamdziko muno ndi umenewu angozolowera.
Timuyi ili pa nambala yachisanu mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 36 pa masewero 24 omwe yasewera mu ligi ya TNM.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores