"KULIKONSE ATITENGEREKO TIKAWACHAPA" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Christopher Nyambose, wati akayambira pomwe anasiyira mu masewero omwe akumane ndi Karonga United kaya pa bwalo lililonse lomwe matimuwa asewerere.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe ali pa bwalo la Rumphi ndipo wati amayembekezera kuti akakumana pa bwalo la Karonga komabe kulikonseko iwo akasewera.
Iye wati timu yake ndiyomwe ikufunikira mapointsi kwambiri kuposa Karonga United ndipo akayesetsa kuti akachita bwino.
"Zokonzekera zayenda bwino kwambiri, tikayambira pomwe tinasiyira ndipo tikayesetsa kuti tikachite bwino chifukwa tikufunikira mapointsi ndi ife kwambiri kuposa anzathuwa." Anatero Nyambose.
Iye watsindikanso kuti timu yake situluka mu ligi poti ali ndi masewero okwana asanu ndi awiri (7) ndipo palibe kutaya mapointsi mpaka asewera mu Airtel Top 8.
Timu ya Chitipa ili pa nambala 15 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 17 pa masewero 21 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores