"TONSE TSOPANO TAGWIRANA" - KAFOTEKA
Mphunzitsi wogwiriza watimu ya FOMO, Elvis Kafoteka, wati tsopano iye ndi anyamata ake adziwana bwino zomwe iwo amafuna ndi zomwenso iye akufuna zomwe zichititse ntchito yake kuyenda bwino.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero ake achiwiri kutsogolera timuyi pomwe akukumana ndi Mighty Tigers pa bwalo la Mulanje ndipo wati wakumana ndi timu ya Osewera abwino kale.
"Zokonzekera zayenda bwino tili ndi timu yabwino yomwe ili ndi osewera abwino kale zomwe zikundipatsa chithunzithunzi kuti tichoka komwe Ife tili. Padakali panopa ndakhalitsano ndadziwana ndi osewera poti zimafunika kudziwana nde tiyesetsa kuti tichoke komwe tili." Anatero Kafoteka.
Iye wati timu yake ili pangozi kwambiri kusiyana ndi timu ya Tigers zomwe ziwachititse kuti asalore Tigers kutenga angakhale point imodzi ku Mulanje.
FOMO ili pa nambala 13 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 18 pa masewero 19 omwe yasewera mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores