BANGWE ITHA KUSINTHA APHUNZITSI
Mkulu komanso wachiwiri kwa mtsogoleri wa timu ya Bangwe All Stars, Chikumbutso Kathumba, wati timu yake ikuunikira mmene aphunzitsi atimuyi akuchitira ndipo ngati kungatheke asintha aphunzitsi atimuyi.
Iye amayankhula ndi wayilesi ya Litala kutsatira mkumano womwe unalipo wokhudza akuluakulu atimuyi komanso aphunzitsi ndipo akhale akutulutsa zotsatira zake lachisanu.
"Masabata amenewa tikuunikira zokonza aphunzitsi atimuyi, padakali pano apereka malipoti ndipo tinali nawo ndi zokambirana lachitatu ndipo zonse tiunikira lachisanu tikamaliza zokambirana." Anatero Kathumba.
Iye anati padakali panopa mwayi ukadalipo wokuti akhonza kuyipulumutsa timuyi kuti isatuluke mu ligi ndipo akufunitsitsa atatero poti akuluakulu nawonso akunyozeka nawo.
Timuyi ili pa nambala 15 mu ligi pomwe ali ndi mapointsi 12 pa masewero 19 omwe yasewera ndipo mu chaka chino chokha yaphunzitsidwa ndi aphunzitsi atatu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores