CHIGAMULO CHA NTAJA RANGERS NDI NYAMBADWE UNITED CHATULUKA
Bungwe loyendetsa ligi yakummwera kwa dziko lino ya Southern Region Football Association latulutsa chigamulo pa nkhani ya masewero omwe matimu a Ntaja Rangers ndi Nyambadwe United anali nawo kamba koti masewero awo sanaseweredwe.
Nkhaniyi ikuti timu ya Nyambadwe United itapita ku Ntaja inavuta kuti bwalo la Ntaja silinalembedwe ndipo iwo sasewera mpaka lilembedwe.
Ena pakhomowa anavomera ndikuyamba kulemba bwaloli ndipo pomwe amamaliza, Nyambadwe inakana kulowa m'bwaloli kenako inakwera bus yawo nkumabwerera ku Blantyre.
Oyimilira timu ya Ntaja pa bwaloli akuti mizere ya pakati pa bwaloli yokha ndi yomwe inafufutika kamba ka mphepo koma anavomera kulemba chomwechonso oyimbira anakamba mofanana.
Chigamulo tsopano chati timu ya Nyambadwe United ikanasewerabe ngakhale sanali okondwa ndipo kamba koti anachoka oyimbira asakudziwa, iwo agonja 2-0 pa masewerowa.
Zateremu Ntaja Rangers yaonjezera mapointsi atatu mu gulu lawo zomw
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores