"TITHOKOZE OYIMBIRA AKUKONZA MPIRA" - KAUNDA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Oscar Kaunda, wadandaula ndi mmene oyimbira achitira pa masewero awo ndi timu ya Blue Eagles mu ndime yamatimu anayi a mpikisano wa FDH Bank ponena kuti agonja kamba ka iwo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-0 kuti atuluke mu chikhochi ndipo wati sangayankhule zambiri poti wawapatsa zigoli a Blue Eagles.
"Anali masewero ovuta kwambiri ndipo timu yathu sinasewere bwino tithokozenso oyimbira powapatsa masewerowa a Blue Eagles akuthandiza kutukula mpira mdziko muno." Anatero Kaunda.
Iye koma wathokoza osewera atimu yake kuti ayesetsa kufika ndimeyi ngakhale ili timu ya Osewera achisodzera ndipo wati chidwi chawo ayika ku ligi ya TNM.
Timuyi tsopano yatuluka mu chikhochi ndipo Blue Eagles ikumana ndi timu yopambana pakati pa timu ya Moyale Barracks komanso FCB Nyasa Big Bullets.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores