"KWAKWANA NDIPO MATIMU TIWALIZA" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Christopher Nyambose, wati timu yake yakonza zolimbikira mmasewero apakhomo ndi cholinga choti azitolera mapointsi omwe akumavuta kuwapeza akayenda.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 4-0 ndi timu ya Bangwe All Stars pa bwalo la Karonga ndipo wachenjeza matimu kuti amva kuwawa akayiyendera timuyi.
"Aliyense akudziwa kuti pomwe tili paja sipakutiyenera nde tikufuna kukhaulitss matimu omwe azibwera pa kwathu poti tikayenda mapointsi akumavuta nde tiwachenjeze matimu kuti amva zowawa zomwe ife timamva tikaluza." Anatero Nyambose.
Iye wayamikira katswiri wawo Trouble Kajani ndi goloboyi wawo watsopano kuti asewera ngati anali kale mutimuyi ndipo akuyembekezera zambiri kuchokera kwa iwo.
Chitipa tsopano ili pa nambala yachikhumi ndi chitatu (13) pomwe ili ndi mapointsi 15 pa masewero 17 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores