"NDI TSIKU LALIKULU KU KARONGA" - KAUNDA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Oscar Kaunda, wati loweruka ndi tsiku lalikulu ku Karonga lomwe anthu amu bomali akuliyembekezera poti lionetsa tsogolo la timuyi mu chikho cha FDH Bank.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Blue Eagles mu ndime ya matimu anayi ndipo wati timuyi yakonza kuti ikapambane koma sizibwera mophweka poti akuyenera kutuluka thukuta.
"Takonzekera bwino kwambiri masewerowa ndipo ili ndi tsiku lalikulu kwa osewera, kwa onse aku Karonga, kwa makolo athu, abale athu ndi ena chifukwa litionetsa tsogolo lathu koma tikufunitsitsa kuti tikapambane koma sizikhala zophweka." Anatero Kaunda.
Iye anatinso timu ya Blue Eagles ili ndi mphunzitsi wabwino yemwe amadziwa ntchito komanso kuti ndi timu yabwino zomwe zitavutitse masewerowa.
Opambana pa masewerowa adzakumana ndi opambana pakati pa matimu a Moyale Barracks komanso FCB Nyasa Big Bullets mu ndime ina ya matimu anayi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores