"TAKONZEKA KUKUMANA NDI KARONGA" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati timu yake yakonzeka bwino kukumana ndi Karonga United mmasewero amu ndime yamatimu anayi mu mpikisano wa FDH Bank loweruka.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe ali pa bwalo la Civo ndipo wati wayesetsa kuwauza osewera ake kulimbikira masewerowa komatu sikuti akhala masewero ophweka.
"Sikuti akhala masewero ophweka chifukwa Karonga United yapano ikusiyana ndi timu yammbuyomu. Iyiyi ikusewera bwino kwambiri zomwe zipangitse kuti tivutike koma tipita ndi mtima wolimbika kuti tikwanilitse khumbo lawo." Anatero Kananji.
Iye wati timuyi yachoka kutali mu mpikisanowu ndipo kufikira pano, maso awo akuyang'ana zogwira chikhochi.
Timu imene idzapambane pa masewero amenewa idzagula malo mu ndime yotsiriza ya mpikisanowu ndipo adzakumana ndi opambana pakati pa FCB Nyasa Big Bullets ndi Moyale Barracks.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores