WANDERERS YATI BULLETS NDE YOKUBA OSEWERAYO
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yaloza chala timu ya FCB Nyasa Big Bullets kuti ndi imene imaba osewera chifukwa yakhala ikuphumitsidwa osewera awiri mmbuyomu.
Mkulu wa timuyi, Panganeni Ndovi, wati timu ya Bullets inawalanda Lloyd Aaron ndi Chawanangwa Gumbo pomwe Manoma anali atapanga kale gawo lalikulu lokambirana ndi matimu awo.
"Izizi kumpira zimachitika. Mwinanso nkhani ya Promise Kamwendo bola Koma Chawanangwa Gumbo anabwera ku Blantyre kunoko kuti akubwera ku Wanderers." Anatero Ndovi poyankhulana ndi nyuzipepala ya Nation.
Izi zikutuluka pomwe matimuwa atengerana ku Football Association of Malawi pomwe Bullets yati inali itapereka kale ndalama pa katswiri wotchedwa Promise Kamwendo yemwe anakasaina mgwirizano ku Wanderers.
Source: Nation
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores