MANOMA AVOMERA KULAKWA KWAWO KU FAM
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yavomereza milandu yomwe inapatsidwa ndi bungwe la Football Association of Malawi kutsatira zachipolowe zomwe timuyi inachita pa masewero omwe inagonja 2-1 ndi FCB Nyasa Big Bullets mu chikho cha FDH Bank mwezi watha.
Mu kalata yomwe timuyi yalemba ku bungweli lati silikufuna kuvutavuta pa nkhaniyi pomwe yavomereza kulakwa kwawo.
Koma timuyi yati ikamapereka chigamulochi iyang'anenso mmene anachitira powaletsa ochemerera awo kusiya kugenda zomwe zinathandizira kuti masewero apitlirebe.
Timu ina ya Karonga United inalandiranso chosagwiritsa bwalo la Karonga kwa masewero atatu komanso kupereka K1 million kamba ka zachiwawa zomwe anachita pomwe ankasewera ndi Mzuzu City Hammers mwezi watha umwewu.
Source: Nation
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores