"CHILANGOCHI NDI CHUMA CHATHU SICHIKUGWIRA" - SIMWAKA
Timu ya Karonga United yati chilango chomwe bungwe la Football Association of Malawi lawapatsa chosasewera masewero atatu pa bwalo lawo ndi chowawa kwambiri kuposa chopereka K1 million poti awononga ndalama zambiri pa masewerowa.
Mlembi wamkulu wa timuyi, Ramzy Simwaka, wati akuluakulu atimuyi akhale akukumana kuti awunikire chilangochi kuti ngati kuli kotheka akasume kuti awachepetsere.
"Mukati muone kukasewera ku Mzuzu ndekuti tiziononga ndalama yokwana K50 million mmasewero amodzi komanso tikakhala pakhomo timatha kupeza ndalama zambiri zapakhomo nde chilangochi chatipweteka kuposa kupereka K1 million." Anatero Simwaka.
Chilangochi chabwera kamba koti ochemerera atimuyi anachita ziwawa pa masewero omwe ankasewera ndi Mzuzu City Hammers mu chikho cha FDH Bank mwezi watha.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores