"ALIYENSE AKUMVA KUWAWA NDI POMWE TILI" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Christopher Nyambose, wati anthu onse ku Chitipa United akumva kuwawa ndi pomwe ali ndipo agwirizana kuthandizana cholinga choti achite bwino mchigawo chachiwiri.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Civil Service United loweruka pa bwalo la Civo ndipo wati akudziwa kuti akhale masewero ovuta koma ayesetsa kuti chigawo chachiwirichi azitolera mapointsi.
"Akhala masewero ovuta kwambiri, mchigawo choyamba tinavutika kwambiri ndipo Civil iyi inatipanganso chipongwe nde tikudziwa akhale ovuta koma tikufuna kuti tizitolera mapointsi angakhale koyenda kuti tichoke komwe tili chifukwa aliyense zikumupweteka kuti tili kumunsi." Anatero Nyambose.
Chitipa United yatsala ndi mapointsi atatu okha kuti ituluke mu chigwa cha matimu otuluka mu ligi pomwe ili ndi mapointsi 12 pa masewero 15 omwe yasewera mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores