"NDI CHILIMBIKITSO KUTHERA MU MATIMU 8 OYAMBA" - KAMWENDO
Mphunzitsi wogwiriza watimu ya Creck Sporting Club, Joseph Kamwendo, wati timu yake imayenera kupambana mmalingana ndi momwe yasewera ndi Premier Bet Dedza Dynamos ndipo chipambanochi ndi chofunikira kwambiri kwa iwo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 2-0 pa bwalo la Aubrey Dimba ku Mchinji lachinayi ndipo wati timu yake yapeza chilimbikitso chachikulu pothera mu matimu asanu ndi atatu oyambilira mu ligi poti ndi timu yaing'ono.
"Ifeyo ndi timu yaing'ono mukudziwa talowa kumene mu ligi koma kuthera mu top 8 mu chigawo choyamba ndi chilimbikitso chachikulu kwambiri kwa anyamatawa poti enawa sanasewerepo ligi yaikulu koma apapa zikuonetsa kuti ndekuti zilibwino." Anatero Kamwendo.
Iye watinso timu yake ikhalebe iwonjezera osewera angapo kutimuyi kuti ayilimbitse ndikuti pamapeto pa ligi izathere pa bwino.
Timuyi yafika pa nambala yachisanu mu ligiyi pomwe ili ndi mapointsi okwana 23 pa masewero 15 omwe yasewera mc
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores