"AKAKHALA MASEWERO OVUTA KOMA TIKAPAMBANA" - KAUNDA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Oscar Kaunda, wamema ochemerera atimuyi kukhamukira pa bwalo la Karonga lamulungu masana poti masewero awo adzakhala kumbali yopambana.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets ndipo wati iwo akonzeka kwambiri koma akufunikira kulimbikira kuti achite bwino.
"Zokonzekera zayenda bwino anyamata akuoneka bwino chatsala ndi kusewera masewerowo koma tikalimbira chifukwa tisatengere chizolowezi kuti pakhomo tikumachita bwino koma tikuyenera kulimbikira kuti tidzachite bwino, tikudziwa adzakhala ovuta koma tidzalimbikira." Anatero Kaunda.
Iye wati timu yake ikuyenera kuchita bwino poti sali pabwino pa ndandanda wa matimu ndipo atatero ndekuti afikira kumtunda kwao.
Timuyi ili pa nambala 11 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 15 pa masewero 13 omwe yasewera mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores