JUST IN:
Timu ya Chitipa United yanyamuka pamodzi ndi osewera wawo wakale, Lorenzo Ghedo yemwe tsopano akufuna akayambe moyo watsopano kumeneku kamba koti nthawi yosewera yachepa ku Bangwe All Stars.
Owinna yapeza kuti osewerayu akhale akumalizitsa zapa pepala kudzera mwa omwe amawayang'anira kuti akatumikire timuyi mu chigawo chachiwiri cha 2024.
Lorenzo anali kale kutimuyi mu 2023 pomwe anapita pangongole kuchokera ku Dedza Dynamos komwe anachita bwino ndipo anathandiza timuyi kuthera pa nambala yachinayi mu ligi.
Osewera angapo tsopano achoka kutimu ya Bangwe All Stars kamba kosowa nthawi yosewera ndipo akusaka matimu ena kuti atumikiremo.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores