"TIMASEWERA NDI WANDERERS YABWINO" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Christopher Nyambose, wati timu yake yakanika kupeza chipambano pamwamba pa timu ya Mighty Mukuru Wanderers kamba koti Manoma anali bwino kuposa iwowo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-0 pa bwalo la Kamuzu ndipo wati timu yake sinachite bwino makamaka mchigawo choyamba ndipo Wanderers inapezerapo mwayi ndikugoletsa zigoli.
"Tagonja zoonadi timasewera ndi timu yoti inali bwino kwambiri ifeyo timatsalira pa mpira komanso pena timachedwa kumaka mpira zomwe zinapangitsa a Wanderers kuti apeze zigoli zawo koma ifeyo tasewera bwino ndipo timuyi poti tikuyimanga tiyesetsa kuti tikonze zinthu kutimuyi." Anatero Nyambose.
Timu ya Chitipa ili pa nambala 14 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 9 pa masewero 13 omwe yasewera mu ligiyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores