"NDI MASEWERO OVUTA KWAMBIRI" - CHIDATI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Civil Service United, Wilson Chidati, wati masewero awo ndi timu ya Creck Sporting Club akhale ovuta poti anyamata onse ndi odziwana komanso amayendera limodzi.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe ali pa bwalo la Civo lachitatu masana ndipo iye wati timu yake yakonzeka kuti ichite bwino pa masewerowa.
"Awa ndi masewero ena osiyana ndi a Bullets aja koma akhala ovuta chifukwa anyamatawa ndi odziwana amayendera limodzi nde tingoona kuti mawali libalanji. Anyamata akuoneka okonzeka kwambiri koma poti ndi mpira zimasintha koma ngati akagwiritse zomwe aphunzitsi tawauza akachita bwino." Anatero Chidati.
Timu ya Civil ili pa nambala yachikhumi ndi chimodzi (11) mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 15 pa masewero khumi ndi awiri (12) omwe asewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores