"IFEYO SI PA MPUNGA PA SILVER" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati timu yawo ifunitsitsa itafika patali mwinanso nkutenga chikho cha FDH Bank ndipo anthu asayiphweketse poti ali ku Chipiku.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Silver Strikers mu ndime ya matimu 32 amu chikhochi ndipo wati iwowa sipampunga pa Silver kamba koti akadali ndi mphamvu.
"Akakhala masewero ovuta kwambiri poti ndi amu chikho nde timu iliyonse imakhala yokonzeka kuti ichite bwino, poti tikumenya ku Chipiku anthu asatichepetse ifeyo tikuyang'ana kuti tikachite bwino koma ndi masewero ovuta kwambiri." Anatero Kananji.
Iye anati timu yawo sinagonjeko mu ligi yawo komanso mu zikho zina zimene asewera pomwenso Silver Strikers sinagonjeko mu TNM Supa ligi zomwe zivutitse masewerowa.
Timu imene ingagonje mmasewerowa omwe adzaseweredwe pa bwalo la Nankhaka udzatulukira mu mpikisanowu ndipo wopambana adzapitilira.
📷: Blue Eagles media
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores