MABEDI ADULIDWA MALIPILO FLAMES IKAMAFABE
Bungwe loyendetsa mpira mdziko muno la Football Association of Malawi lati mphunzitsi watimu ya dziko lino, Patrick Mabedi, atha kuchotseredwa ndalama zokwana K10 pa K100 iliyonse ngati timu ya Flames ipitilire kusachita bwino.
Izi zadza pomwe timuyi yagonja 1-0 ndi Equatorial Guinea koyenda sabata yatha mu masewero opitira ku World Cup ya 2026 ndipo bungweli lati Mabedi akuyenera kutsogolera timuyi kuti izichita bwino.
Masabata apitawa, bungweli linati liunikiranso mgwirizano wake ndi mphunzitsiyu kuti awone zina zomwe anapatsidwa kuti akwanilitse ali pa ntchitoyi poti anasayina pansi pa mtsogoleri wa kale, Dr Walter Nyamilandu Manda.
Chipatsidwireni mgwirizano wake wa zaka ziwiri, timuyi yakwanitsa kungopambanako masewero awiri okha basitu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores