"GABADINHO WAKE WAKALAMBAYO NDE UTI?" - WADABWA KHUDA
Katswiri wakale watimu ya Silver Strikers, Khuda Muyaba, wadabwa ndi mfundo ya mphunzitsi watimu ya Malawi, Patrick Mabedi yonena kuti Gabadinho Mhango wakula ponena kuti ndi bodza.
Iye wayankhula izi kutsatira kusiyidwa kwa katswiriyu ndipo wati iye amanenedwa kuti amayankhula kwambiri koma amadziwa kuti Mabedi ndi wolakwika kwambiri.
"Gaba Sanakalambe. Ine ndili ndizambiri zokamba, nkaona bwino ndilankhula bola musati ndimalankhula udyo." -Watero Khuda.
Muyaba analumbilira kuti sadzaseweranso pansi pa Mabedi ponena kuti samadziwa kuphunzitsa komanso amadana ndi osewera ena.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores