MZUZU CITY HAMMERS ILI PAMWAMBA PA LIGI
Timu ya Mzuzu City Hammers ikupitilira kuchita bwino pomwe yapambana masewero awo achiwiri mu ligi pogonjetsa Baka City 2-1 pa bwalo la Mzuzu.
Isaac Msiska komanso Yasin Rashid anamwetsa zigoli zatimuyi pomwe Joseph Mwambungu anapeza chopukutira misonzi zomwe zinakondweretsa mphunzitsi wamkulu, Elias Chirambo.
"Ndine wokondwa kwambiri kamba koti tapambana, sabata yatha tinavutika popita kutsogolo nde tinakonza mavuto athu, tasewera bwino ndipo tapambana. Sine wokhutira ndi mipata yomwe taphonya poti tinakonza kwambiri kutsogolo nde tikakonzanso." Anatero Chirambo.
Hammers tsopano ili pamwamba pa ligi ndi mapointsi asanu ndi imodzi (6) omwe awapeza pa masewero awiri omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores