SUPA LIGI IYAMBA PA 6 APRIL
Mpira ukuyembekezeka kubwereranso pa bwalo la zamasewero posachedwa pomwe TNM Supa ligi ikuyembekezeka kuyamba pa 06 April malingana ndi dongosolo lomwe Football Association lapanga.
Mwa zina, timu yadziko lino ya Flames ichita m'bindikiro wake wokonzekera masewero opitira ku World Cup ya 2026 kuyambira pa 28 February kukafika pa 18 March 2023.
Masewero mdziko muno adzayamba pa 30 March 2024 ndi Charity Shield pomwe zikuyembekezeka kuti matimu a FCB Nyasa Big Bullets, MAFCO, Silver Strikers komanso Mighty Mukuru Wanderers akumveka kuti adzasewera mu mpikisanowu.
FCB Nyasa Big Bullets ndi imene ikuteteza zikho zonse zomwe zili mdziko muno.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores