AZUNGU AKUTHAMANGIRA KU WANDERERS
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers ikuyembekezeka kulengeza mphunzitsi watsopano kutimuyi pasanafike pa 16 February 2024 pomwe zaonetsa kuti azungu ochuluka akufunitsitsa ntchito ku Manomaku.
Izi zadza pomwe mkulu watimuyi, Roosevelt Mpinganjira, watsimikiza kuti azungu ochoka ku ulaya 15, amu Africa mommuno koma mayiko ena 7 komanso aku Malawi kuno atatu ndi omwe alembera ntchito tsopano.
Iye wati kusapezeka kwa amalawi angapo ndi chifukwa choti maphunziro awo akuchepa ndi mphamvu za timuyi.
"Ndi zoona atatu okha ndi omwe alembera [aku Malawi] komatu chifukwa choti Wanderers ndi dzina lalikulu kwambiri ndipo limafunika ukadaulo ndiye aku Malawi kuno sakufikira pa mulingo watimuyi." Anatero Mpinganjira.
Manoma alibe mphunzitsi kutsatira kuchoka kwa Mark Harrison yemwe anatsanzika kutimuyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores