"MWANA UJA ATENGA MAULEEE" - ABAMBO
Mwini wake watimu ya Mighty Tigers, Robin Alufandika, watsimikiza kuti goloboyi watimuyi, Innocent Nyasulu, wagulitsidwa ndi timuyi kupita ku FCB Nyasa Big Bullets.
Alufandika ati za mtengo sakudziwa kamba koti iwo angouzidwa kuti malonda atheka ndipo amufunira zabwino katswiriyu.
"Ndikhoza kutsimikiza kuti Maule atenga atenga mwana wabwino uja. Za ndalama sindikudziwa poti maofesi ndi otseka koma angondiuza kuti mwana wabwino uja basi Maule atenga." Anatero Abambo.
Koma wamkulu kutimu ya Bullets, Sugzo Nyirenda anati chimene akudziwa ndi choti matimuwa amakambirana zakatswiriyu ndipo zikatheka atsimikiza ku mtundu wa a Malawi.
"Ndi zoona timakambirana nawo koma zoti wabwera ku Bullets sindingatsimikize mwina akadzasaina mgwirizano ndi pomwe ndidzakhale ndi mphamvu kuyankhula." Anatero Nyirenda.
Nyasulu ndi goloboyi yemwe anagwirira bwino mu ligiyi pomwe wasankhidwa nawo pagulu la osewera omwe achita bwino mu ligiyi ndipo sanachinyitseko mmasew
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores