"NDITHOKOZE MULUNGU NDABWERA KUTIMU YAIKULU" - LAMECK
Katswiri yemwe wangosaina mgwirizano ndi timu ya Silver Strikers, Macdonald Lameck, wati akhala osewera olimbikira kwambiri chifukwa ochemerera atimu yaikulu amafuna zipambano zokhazokha basi.
Iye amayankhula pomwe amatikitira mgwirizano wa zaka zitatu kumalizitsa za kuchoka kwake kutimu ya Blue Eagles. Iye wati Blue Eagles inamusamalira kwambiri ndipo zinamutsegulira mwayi wochita bwino.
"Ndithokoze Mulungu pondipatsa mwayi woti ndisewere timu yaikulu ngati Silver ndipo ndikukhulupilira kuti ndichita bwino kwambiri.Kusewera timu yaikulu ngati Silver chimafunikira kwa masapota ndi chimodzi basi, kupambana." Anatero Lameck.
Katswiriyu anachokera ku FCB Nyasa Big Bullets kuti apiteko ku Blue Eagles komwe wasewera zaka ziwiri ndipo mu nthawiyi watumikirakonso timu ya Flames.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores