HARRY NYIRENDA NDI ENA ACHOTSEDWA KU CIVO
Team ya Civil Service United FC yachotsa osewela asanu ndi awiri pomwe ikufuna kuyamba zokomzekera zawo.
Malingana ndi mlembi wa team ya Civil, Edgar Chipalanjira wauza wayilesi ya Kasupe mmawa wa lachinayi kuti ndizoona achotsadi anyamatawa omwe alipo 7.
Osewelawa ndi Luke Chima, William Bwetu Mwalwimba, Harry Nyirenda, Frank Banda, Sugzo Mwakasinga, Dan Kumwenda ndi Innocent Tanganyika.
Chipalanjira wati osewera Innocent Tanganyika akhale akuthandiza team yachisodzela ya Civil.
Posachedwapa, mlembi wa Civil adaululaso kuti osewera wawo Lloyd Banega Aaron akhale akulowela ku team ya FCB Nyasa Big Bullets.
Wolemba : Gift Tembo
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores