"TAYIWALA ZA KULUZA NDI DEDZA APA TIPANGE ZA LERO" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wati timu yake yaiwala kale za kugonja kwawo ndi Dedza Dynamos ndipo akonzekera bwino kukumana ndi Blue Eagles.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe akumane mu ndine ya matimu anayi amu Airtel Top 8 pa bwalo la Bingu ndipo wati osewera ake akudziwa kufunikira kopambana masewerowa.
"Ndi masewero ofunikira kwambiri, ndi amu chikho nde tiwatenga kuti akatheretu pompo, tawauza osewera athu za kufunikira kwa masewero amenewa ndikukhulupilira kuti akachita bwino. Tikukumana pa bwalo loti tonse ndi koyenda nde sitikudziwa kuti iwo akonza motani komabe tiyesetsa kuti tipambane." Anatero Munthali.
Iye watinso osewera ena sapezeka kamba koti mphamvu akadalibe koma ambiri alibwino. Opambana mmasewero amenewa azigulira malo oyamba a ndime yotsiriza yamu chikhochi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores