SULOM YASUNTHA MASEWERO A BULLETS NDI KARONGA
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets ikuyenera kusewera ndi timu ya Blue Eagles lamulungu kenako kunyamuka kupita ku Karonga kuti akakumane ndi Karonga United lachitatu pomwe bungwe la Super League of Malawi lasuntha masewero awo.
Masewero a matimu awiriwa amayenera kuseweredwa lachinayi pa 30 Novembala 2023 koma bungweli laika masewerowa pa 29 Novembala kuti matimuwa asewere masewero awo achi 29.
Bullets ili ndi mapointsi 56 pa masewero 28 omwe yasewera mu ligiyi ndipo ili pa nambala yoyamba pomwe Karonga ili ndi 37 points pa masewero 28 ndipo ili pa nambala yachisanu ndi chitatu (8).
Mu chigawo choyamba, timu ya FCB Nyasa Big Bullets inapambana 2-0 mmasewero omwe anakumana pa bwalo la Kamuzu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores