BAKA CITY YALOWA MU SUPA LIGI
Timu ya Baka City yaku Karonga yakhala akatswiri a chikho cha SIMSO and Innobuild Northern Region Football League angakhale kuti kwatsala masewero awiri pomwe yagonjetsa Ekwendeni United 2-1 loweruka.
Timuyi yasewera masewero 12 mu ligiyi pomwe yapambana masewero 9 kufanana mphamvu kamodzi komanso kugonja kawiri kuti ipeze mapointsi 28 omwe palibe timu imene ingafikire mu ligiyi.
Timu ya Embangweni United ili pachiwiri ndi mapointsi 21, Kadona Stars ili pachitatu ndi 20 pointsi pomwe Iponga ili pachinayi ndi mapointsi 18. Mzimba United ndi Ekwendeni United ali pachisanu ndi pachisanu ndi chimodzi ndi mapointsi 16 pomwe Mayamiko Stars ili ndi mapointsi 9 ndipo Ekwendeni Hard Knockers ili ndi mapointsi 7.
Ngati matimu akumpoto onse a Moyale Barracks ndi Ekwendeni Hammers angapulumuke mu ligi, kukhala matimu asanu ku chigawochi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores