"TIMAFUNITSITSA KUWINA KOMA TINGOVOMEREZA BASI" - MPINGANJIRA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Albert Mpinganjira, wati timu yake yataya mapointsi ofunikira kwambiri omwe akanatha kuwathandiza kuonjezera mwayi wotenga ligi.
Iye amayankhula izi atatha masewerowa omwe alepherana 0-0 ndi Mighty Wakawaka Tigers pa bwalo la Kamuzu ndipo wati mavuto otaya mipata yochuluka ndi omwe akanikitsa kupambana.
"Ndi zoonadi masewerowa anali ofunikira kuti tipambane komabe takanika tingovomereza kuti zavuta tiona mmasewero omwe tatsala nawo. Ndi vuto lachizolowezi lophonya kwambiri komabe zimachitika mu mpira, tingovomereza kuti zatero." Anatero Mpinganjira.
Timuyi ikanapambana, ikanafika pa nambala yoyamba mu ligiyi koma tsopano ili pa nambala yachitatu ndi mapointsi 55 pa masewero 29 ndipo ikufunikira kuti Bullets idzagonje ndi Karonga United ndi kufanana mphamvu ndi Silver Strikers kuti itenge ligi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores