"INALI PLAN YATHU KUIKHUMUDWITSA WANDERERS" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Christopher Nyambose, wati amadziwa kuti masewero awo ndi Mighty Mukuru Wanderers akhala ovuta kwambiri potengera kuti matimu onse amafunitsitsa mapointsi atatu.
Iye amayankhula atatha masewero omwe matimuwa alepherana 0-0 pa bwalo la Kamuzu ndipo wati anyamata ake anachita zomwe anawauza kuti angowakhumudwitsa a Wanderers.
"Anali masewero othamanga kwambiri komanso ovuta kwambiri poti matimu onse amafunitsitsa chipambano. Ife tikuthawa kuti tisatuluke mu ligi komanso Wanderers imafuna kuti mwina ikokere chikho ku Lali Lubani komabe anyamata asewera bwino mpaka tatengako point imodzi." Anatero Nyambose.
Timu ya Tigers ili pa nambala 10 mu ligiyi ndi mapointsi 35 pa masewero 29 omwe yasewera ndipo yatsala kuti ikumane ndi timu ya Kamuzu Barracks koyenda kuti amalize ligi ya chaka chino.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores