FLAMES IKADALI PA NAMBALA 123
Timu ya dziko lino ya Flames sinasuntheko pa ndandanda wa matimu a padziko lonse la pansi pomwe yaimabe pa nambala 123 pa dziko lonse mu ndandanda womwe watuluka lachinayi.
Timuyi yasewera masewero awiri mu November pomwe yagonjetsa timu ya Liberia 1-0 kuyenda koma inagonja pakhomo ndi Tunisia 1-0.
Mwezi wa December ukhale mwezi wachisanu timuyi kukhala pa nambalayi yomwe anakhalitsaponso nthawi yomwe ankapitsa ku mpikisano wa 2021 African Cup of Nations chaka chathachi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores