MASEWERO A WANDERERS NDI SILVER ASUNTHIDWA
Bungwe la Football Association of Malawi lasuntha masewero amu chikho cha Airtel Top 8 achibwereza pakati pa matimu a Mighty Mukuru Wanderers ndi Silver Strikers kamba koti milandu ikadakambidwabe.
Bungweli lalengeza za izi lachitatu kutsatira kusuma kwa Wanderers kachiwiri kamba kosakhutira ndi chigamulo chomwe bungweli linapereka kutimuyi.
Iwo ati mbali zokhudzidwa pa nkhaniyi amayenera kukambira pa 21 November koma kamba ka zifukwa zina, akumana pa 24 November zomwe zikutanthauza kuti pa 25 November chiganizo chikhala chisanapangidwe.
Timu ya Wanderers ikukana chiganizo choti inagonja 2-0 kamba koti inakana kumalizitsa masewero oyamba ku Lilongwe komanso kuti ilipire K24.5 million kamba kophwanya mipando pa bwalo la Bingu.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores