"ATOLANKHANINU ANGAKUUZENI KUTI MWAKULA SIYANI KULEMBA NKHANI" - BANDA
Mtsogoleri watimuyi ya Flames, John Banda, wati nthawi yake sinakwane yoti asiye kusewerera timu ya dziko lino pomwe wati iye ndi akuluakulu ena akuthandiza achisodzera kuti akhazikike bwino mu timuyi.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero atimuyi ndi Tunisia lachiwiri likudzali pa bwalo la Bingu ndipo wati iye monga ntchito yake ndi kusewera mpira, iye agwirabe ntchito yakeyo.
"Amene amasankha osewera ndi kochi osati ine nde ngati kochi wakonda kuti ndigwire ntchito ndikuyenera kutero ndithu, iyi ndi ntchito yathu, atolankhani palibe angakuuzeni kuti mwakula siyani kulemba nkhani, ndi ntchito yanu." Anatero Banda.
Iye wati osewera onse atimuyi akonzekera bwino lomwe kuti akalimbikire ndi kugonjetsa timu ya Tunisia. Katswiriyu ali ndi zaka 30 ndipo anayamba kusewera timuyi zaka 12 zapitazo mu nthawi ya Kinnah Phiri.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores