WANDERERS YAUMITSABE MTIMA
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yati ikasumanso kachiwiri pa chiganizo cha timuyi kamba koti bungwe la Football Association of Malawi silinachite kalikonse pa dandaulo lawo la poyamba.
Timuyi inasuma itapatsidwa chilango kuti ilipire K24.5 million komanso kuti inagonja 2-0 ndi Silver Strikers mmasewero awo a Airtel Top 8 koma bungweli silinasinthepo kalikonse.
Mmodzi mwa akuluakulu atimuyi, Chancy Gondwe, wati timuyi yachita chiganizo chokasumanso.
"Tikati tiunikire pa chigamulo choyamba chija ndi ichi palibe chimene chasinthapo nde ifeyo zomwe tinanena sizinamveke." Anafotokoza Gondwe.
Timuyi imayenera kusewera ndi Silver Strikers mu masewero achibwerenza loweruka sabata ya mawa pa 25 November koma zateremu mpikisanowu uchedwa kaye poti atha kulepherekanso.
Source: wa mpira
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores