WANDERERS YAFIKA MU NDIME YA MATIMU 16 MU CASTEL
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yavutika komabe yafika mu ndime ya matimu khumi asanu ndi mmodzi (16) achikho cha Castel Challenge Cup kutsatira kugonjetsa timu ya FOMO 1-0 pa bwalo la Kamuzu lachinayi.
Katswiri wa timuyi, Chiukepo Msowoya, anachita kuchokera panja kuti agoletse chigoli chopambanira atasumbira mpira womwe anamenya Madinga pa mphindi 85.
Wanderers inavuta mchigawo choyamba pomwe FOMO inapanikiza kwambiri koma Christopher Kumwembe, Francisco Madinga, Isaac Kaliati ndi Felix Zulu analowa mmalo mwa Francis Mkonda, Vincent Nyangulu, Emmanuel Nyirenda ndi Robin Ngalande ndi pomwe inasintha.
Chiukepo analowa mmalo mwa Misheck Botomani pa mphindi 80 za masewerowa ndipo mphindi zisanu zinali zokwana kupeza chigoli chake chachinayi cha mpikisanowu.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores