PHIRI WAPAMBANA MPHOTO KU BULLETS
Katswiri wa timu ya FCB Nyasa Big Bullets, Precious Phiri, wasankhidwa kukhala wosewera wapamwamba kuposa aliyense mu mwezi wa September kutimuyi.
Timuyi yalengeza za nkhaniyi lachiwiri masana pomwe katswiriyu wapeza mavoti ochuluka kuposa osewera ena anzake, Ernest Petro komanso Patrick Mwaungulu.
Phiri wakhala ofunikira kwambiri pomwe amalowa mmalo a osewera omwe amavulala ndipo wasewerapo ngati wotseka kumbuyo kumanja komanso kumanzere, wapakati ndi mmbali.
Iye anapita kutimuyi mu 2018 atamugula kuchokera ku Mighty Tigers ndipo wapambana zikho za TNM Supa ligi kuchokera mu 2018 mpaka pano.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores