WANDERERS YALEMBERA FAM ZINTHU 19 ZOLAKWIKA KUPHATIKIZA NKHAKANANGA
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yalembera kalata bungwe la Football Association of Malawi yoonetsa kusakondwa ndi mmene oyimbira Godfrey Nkhakananga anayimbilira mmasewero awo ndi Silver Strikers pa bwalo la Bingu loweruka latha.
Mu kalata imene yasainidwa ndi mkulu woyang'ana za milandu, Chancy Gondwe, watchulamo zifukwa 19 zimene timuyi sinakondwere ndi kuimbira pa masewerowa. Iwo ati kupitira kwa masewero kumaonetsedwa ndi manja osati wezulo ndipo osewera a Silver amayenera kulandira makadi kamba komenyabe mpira.
Iwo ati oyimbira akaimba mwatsoka amauponya mpira pansi zomwe sizinachitike ndipo ataimbamo osewera atimuyi ena anasiya kumaka pomwe ena anachepetsa kamakidwe. Iwo atinso zomwe analemba Nkhakananga zoti "Nyerere azithira seven-seven ku Zomba." zikuonetsa kuti anachita dala.
Iwo ayikamonso malamulo ena a FIFA ndipo ati akukhulupilira kuti FAM itsatira chilungamo pa nkhaniyi. Nkhakananga anaimba kuti osew
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores