"CHINACHAKE SICHILI BWINO KWA ANYAMATA ATHU" - MTETEMERA
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, MacDonald Mtetemera, wati akhulupilira kuti pali chinthu chomwe chalakwika kwa anyamata ake pomwe wati palibe yemwe anasewerako bwino mmasewero omwe agonja 2-0 ndi Kamuzu Barracks.
Iye amayankhula izi atatha masewerowa pa bwalo la Kasungu pomwe wati afufuza chimene chachitika kwa osewera atimuyi pomwe wati KB yasewera bwino komanso anyamata ake sanali bwino.
"Lerolo chimene ndingayankhule ndi chakuti zabwino zonse kwa Kamuzu Barracks, lero anyamata anga onse sanali bwino. Mwina pali mavuto omwe ngati aphunzitsi tikuyenera kuwafufuza chifukwa kulekerera ndekuti zitivuta komabe tiyesetsa tikhale nawo pansi tifufuze." Anatero Mtetemera.
Timu ya Chitipa ikanapambana ikanafika panambala yoyamba mu ligi koma tsopano ikhalabe pa nambala yachitatu ndi mapointsi 39 pa masewero 22 mu ligi.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores