"UDZU WAKE NDI WAKUNYUMBA OSAYENERA PA BWALO LA MPIRA" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Christopher Nyambose, wati timu yake inavutika kuti isewere bwino pa bwalo la Rumphi kamba koti kapinga yemwe ali pa bwaloli amatelera kwambiri.
Nyambose amayankhula izi atatha masewero omwe analepherana 1-1 ndi timu ya Ekwendeni Hammers ndipo wati point yomwe atengayi iwathandiza kusokerera penapake pofunikira.
"Anali masewero abwino anyamata anayesetsa kuti asewere bwino koma kapinga ali pa bwaloli ndi uja amafunika kukhala kunyumba uja nde amatelera mwina pakufunikira kapinga uja ogwira uja kuti pasamatere. Ligi yavuta ndipo point iliyonse ikumakhala yofunikira kwambiri, point yalero itisuntha penapake." Anatero Nyambose.
Timu ya Tigers ili tsopano ndi mapointsi 28 pa masewero 24 omwe yasewera mu ligiyi ndipo ili pa nambala yachikhumi.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores