"TIKUFUNIKIRA KUTI TIZIWINA MASEWERO OMWE ATSALA" - CHIDATI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Civo United, Wilson Chidati, wati timu yake ikufunikira kuti izipambana masewero aliwonse omwe atsala nawo ndi cholinga choti atsalebe mu ligi ya TNM.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe analepherana 1-1 ndi timu ya Karonga United ndipo anati timu yake inazizira kwambiri kutsatira kuima kwa masewerowa kwa pafupifupi mphindi makumi awiri koma wati amayenera kuwina.
"Anali masewero abwino kwambiri 50-50 mmene ndinanenera muja, tinasewera bwino mchigawo choyamba mpaka tinapeza chigoli koma mchigawo chachiwiri anzathuwa anabwera mwa mphamvu ndipo ndikuima kwa masewero tinazizizira nde mnyamata wawo analowa uja anapeza chigoli. Za oyimbira, chiganizo chake ndi chomaliza nde tiyeni tizisiye." Anatero Chidati.
Civo tsopano yatuluka ku chigwa cha matimu otuluka pomwe ili pa nambala 13 ndi mapointsi 25 pa masewero 22 omwe yasewera.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores