"OYIMBIRA SANAONE ZOLAVULILIDWAZO" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Trevor Kajawa, wati oyimbira Kondwani Kamwendo, sanalakwitse kuchotsa kalata yofiira ya Katswiri wawo, Allen Chihana, kamba koti analibe umboni okwanira oti katswiriyu analavuliradi osewera wa Civo.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe analepherana 1-1 ndi Civo ndipo masewerowa anaimba kwa pafupifupi mphindi makumi awiri kutsatira Karonga kukana kalatayi kuti ilibe umboni. Iye wati Civo inangomuuza oyimbira zabodza poti katswiriyu amawazunguza.
"Sindikufunapo kuyankhula zambiri koma ndi zoti oyimbira anali zoti sanazione anangouzidwa basi nde ndikuona kuti a Civo anapanga dala chifukwa Allen anali kuti akukwavutitsa kwambiri nde amafuna atuluke koma anali masewero abwino, Civo yasewera bwino mchigawo choyamba ife chachiwiri." Anatero Kajawa.
Timu ya Karonga United ikadali pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) pomwe ili ndi mapointsi 32 pa masewero 23 amene yasewera.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores