MADISE WAPITA PA NGONGOLE KU GREEN BUFFALOES
Katswiri watimu ya Scorchers, Chimwemwe Madise, wapititsidwa pa ngongole ku timu ya Green Buffaloes yaku Zambia pamodzi ndi osewera awiri anzake akutimu ya Elite Ladies kuti akathandize timuyi pa mpikisano wopitira ku mpikisano wa CAF Women's Champions league omwe useweredwe kuyambira pa 30 August.
Timu ya Elite Ladies yatsimikiza za nkhaniyi mmawa wa lachisanu pomwe yati matimu awiri asainirana mgwirizano wa ndalama yokwana K30,000 yaku Zambia komweko. Elite yapereka osewerawa ngati njira imodzi yothandizira Buffaloes ku mpikisanowu pomwe ikuimilira Zambia.
Timuyi yati katswiriyu pamodzi ndi Comfort Selemani ndi Xiomara Mapepa azitumikirabe timu yawo mu ligi ya FAZ Women's Super League ndipo Green Buffaloes itha kufuna ntchito zawo mu ligi ya chaka cha mawa. Ngati timuyi ikafike ku mpikisano wa Champions league, osewerawanso adzasewerera Buffaloes.
Mapepa ndi Selemani anali limodzi ndi timu ya Zambia ku mpikisano wa World Cup pomwe Madi
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores