MADINGA ATHA KUONEKA LERO
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers itha kukhala ndi osewera wawo, Francisco Madinga, lero pomwe akukumana ndi timu ya Santhe ADMARC pa bwalo la Kamuzu pomwe mphunzitsi watimuyi watsimikiza kuti kalata yovomereza kusewera mdziko muno kuchokera kunja yafika.
Mark Harrison wati mwina chitupa chosewerera masewero chake chipangidwa lero ndipo saganizangati Kaye ngati amuseweretse makamaka masana alerowa.
Madinga wasaina mgwirizano wa zaka ziwiri kutimuyi pomwe wabwereranso kutsatira kutha mgwirizano ndi timu ya Dila Gori FC ndipo katswiriyu sankafuna kuonjezera mgwirizano wakewu atazindikira kuti akulandira ndalama yochepa kwambiri.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores