CHAWINGA AKUFUNIDWA NDI ARSENAL KOMANSO ENA AWIRI
Katswiri wa Scorchers, Tabitha Chawinga, akufunidwa ndi timu yaku Mangalande, Arsenal komanso PSG yaku France ndi Roma yaku Italy pomwe wabwereranso kutimu ya Wuhan Jiangda yaku China.
Nyuzipepala ya Times yasindikiza za nkhaniyi ponena kuti matimuwa akopeka mtima ndi osewerayu pomwe anachita bwino ndi timu ya Inter Milan yomwe ankasewera pa ngongole mu ligi yangothayi pomwe anakhala katswiri womwetsa zigoli zochuluka ndi zigoli 23.
Inter inakanika kumuguliratu katswiriyu pomwe mu mgwirizano wawo wa ngongole, Wuhan, inakana kuti katswiriyu akasewerenso timu Ina mu ligi ya chaka cha 2023 mpaka 2024.
Arsenal ndi imodzi mwa matimu akuluakulu ku Mangalandeko pomwe inathera mu ndime ya matimu anayi mu UEFA champions league ndipo Roma anakhala akatswiri a chikho cha ku Italy. Nawo PSG ndi timu yaikulu ku France yomwe imasinthanasinthana zikho ndi timu ya Olympic Lyonnais.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores