EMILY JOSSAM WA BULKETS WAPITA KU ZESCO
Katswiri wotseka kumbuyo ku timu ya FCB Nyasa Big Bullets yosewera mpira wamiyendo koma ali amayi, Emily Jossam, tsopano asewera mu FAZ Women's Super Division ku Zambia pomwe wapita kutimu yaku Ndola, Zesco United.
Jossam anali mtsogoleri wa Bullets ndipo wapita pa mgwirizano wokhazikika ndi Zesco pomwe anaithandiza timu yake mmasewero osiyanasiyana mu zikho mdziko la Malawi.
Iye wasewera kale masewero atimuyi ku Congo komwe anagonja 2-0 ndi timu yomwe amasewera Sabina Thom, TP Mazembe ku Lubumbashi dzina ndipo matimuwa akumananso lero mmasewero ena awubale.
Emily watsatira osewera ena aku Malawi monga Chimwemwe Madise ndi Madyina Ngulube a Elite Ladies komanso Wezzie Vitumbiko Mkandawire ndi wotchinga pagolo, Ruth Mhango a Zambia Institute for Sustainable Development (ZISD).
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores